Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 24:46 - Buku Lopatulika

46 Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 Chidzakhala chabwino kwa wantchitoyo ngati mbuye wake pofika adzamupeza akuchita zimenezi.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:46
10 Mawu Ofanana  

Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?


Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zake zonse.


Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:


Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.


Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero.


(Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)


Ndidziwa ntchito zako, ndi chikondi, ndi chikhulupiriro, ndi utumiki, ndi chipiriro chako, ndi kuti ntchito zako zotsiriza zichuluka koposa zoyambazo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa