Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 22:44 - Buku Lopatulika

44 Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale padzanja lamanja langa, kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale pa dzanja lamanja langa, kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 “ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja, mpaka nditasandutsa adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 “Ambuye anati kwa Ambuye wanga: ‘Khala pa dzanja langa lamanja mpaka ndiyike adani ako pansi pa mapazi ako.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 22:44
20 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.


Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwake, ndipo moto udzawanyeketsa.


Chifukwa chake ngati Davide amtchula Iye Ambuye, ali mwana wake bwanji? Ndipo panalibe mmodzi anatha kumyankha mau.


Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.


Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Tomasi anayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.


kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala mu Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu:


Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake.


Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu,


Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala padzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako?


ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,


Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.


Ndipo ndinaona chilombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa