Mateyu 22:4 - Buku Lopatulika4 Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsa: idzani kuukwati. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsa: idzani kuukwati. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Idatumanso antchito ena nkunena kuti, ‘Kaŵauzeni oitanidwa aja kuti chakudya chakonzeka. Ndapha ng'ombe ndi nyama zina zonenepa. Zonse zakonzeka, bwerani ku phwando laukwati.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 “Kenaka anatumiza antchito ena nati, ‘Awuzeni oyitanidwa kuti phwando lakonzedwa: ndapha ngʼombe yayimuna ndi nyama zina zonenepa ndipo zonse zakonzedwa. Bwerani ku phwando laukwati.’ Onani mutuwo |