Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:34 - Buku Lopatulika

34 Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Nyengo yothyola zipatso itayandikira, munthu uja adatuma antchito ake kwa alimi aja, kuti akatengeko zipatso za m'munda muja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Pamene nthawi yokolola inakwana, anatumiza antchito ake kwa matenanti aja kuti akatenge zipatso zake.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:34
20 Mawu Ofanana  

Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wampesa, chimene sindinachite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya?


Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yake yoipa, konzani machitidwe anu, musatsate milungu ina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunanditchere khutu lanu, simunandimvere Ine.


Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala.


Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.


Tsono atabwera mwini munda, adzachitira olimawo chiyani?


Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake.


natumiza akapolo ake kukaitana oitanidwa kuukwati umene; ndipo iwo sanafune kudza.


Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wampesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.


Koma olima ajawo, ananena mwa iwo okha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu.


Pamenepo mwini munda adzachita chiyani? Adzafika, nadzaononga olimawo, nadzapereka mundawo kwa ena.


Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wampesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa