Mateyu 21:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Ataona mkuyu pambali pa mseu, nkupitapo, sadapezepo chilichonse koma masamba okhaokha. Pamenepo adauza mtengowo kuti, “Mtengo iwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya usadzabalenso konse zipatso.” Nthaŵi yomweyo mkuyu uja udachita kuti gwa, kuuma. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, “Usadzabalenso chipatso!” Nthawi yomweyo mtengowo unafota. Onani mutuwo |