Mateyu 20:30 - Buku Lopatulika30 Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'mphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anafuula nati, Mutichitire ife chifundo, Inu Mwana wa Davide. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201430 Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'mphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anafuula nati, Mutichitire ife chifundo, Inu Mwana wa Davide. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa30 Panali anthu aŵiri akhungu amene adaakhala pansi pamphepete pa mseu. Iwo aja atamva kuti Yesu akupita mumseumo, adayamba kufuula kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero30 Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!” Onani mutuwo |