Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 2:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 “ ‘Iwe Betelehemu wa m'dziko la Yuda, sindiwe wamng'ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda. Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri pamene adzalamulira anthu anga Aisraele.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 “ ‘Koma iwe Betelehemu, chigawo cha Yudeya, sindiwe wamngʼonongʼono mwa olamulira a Yudeya; pakuti otsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraeli.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 2:6
24 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.


Salima atate wa Betelehemu, Harefi atate wa Betegadere.


Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ake, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);


Ana a Betelehemu zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu.


Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Ndipo wina wotuluka mu Yakobo adzachita ufumu; nadzapasula otsalira m'mizinda.


Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,


Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.


Ananena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga.


Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?


ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamutu pa zonse, kwa Mpingo


Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba.


Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


ndipo adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga Inenso ndalandira kwa Atate wanga;


chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa