Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 2:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anamuuza iye, Mu Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anamuuza iye, M'Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Iwo adati, “M'mudzi wa Betelehemu ku Yudeya. Pajatu mneneri adalemba kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo anamuyankha kuti, “Ku Betelehemu wa ku Yudeya chifukwa izi ndi zimene mneneri analemba kuti,

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 2:5
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anafa Rakele, naikidwa panjira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu).


Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,


Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe aakulu onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Khristuyo?


Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?


ndi Katati, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: mizinda khumi ndi iwiri ndi midzi yao.


Ndipo panali mnyamata wa ku Betelehemu ku Yuda, wa banja la Yuda, ndiye Mlevi, nagonera iye komweko.


Ndipo masiku akuweruza oweruzawo munali njala m'dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu ku Yuda anamuka nakagonera m'dziko la Mowabu, iyeyu, ndi mkazi wake, ndi ana ake aamuna awiri.


Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi?


Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.


Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera mu Efurata, numveke mu Betelehemu;


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa