Mateyu 19:12 - Buku Lopatulika12 Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Paja pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa adabadwa motero. Pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa anthu adaŵafula. Pali enanso amene adachita kusankha okha kusakwatira, kuti azitumikira bwino Mulungu. Yemwe angathe kumvetsa, amvetse.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Pakuti ena ndi akuti sangakwatire chifukwa anabadwa motero, ena ali motero chifukwa chofulidwa ndi anthu ndipo ena anawukana ukwati chifukwa cha ufumu wakumwamba. Iye amene angalandire ichi alandire.” Onani mutuwo |