Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 16:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse chizindikiro cha Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse chizindikiro cha Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsiku lina kudabwera Afarisi ndi Asaduki ena kwa Yesu. Adampempha kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba. Pakutero ankangofuna kumutchera msampha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Afarisi ndi Asaduki anabwera kwa Yesu ndi kumuyesa pomufunsa kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 16:1
33 Mawu Ofanana  

Yankha chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti asadziyese wanzeru.


Ndipo Afarisi anatuluka, nakhala upo womchitira Iye mwa kumuononga.


Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ochokera ku Yerusalemu, nati,


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki.


Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chilichonse?


Pomwepo Afarisi anamuka, nakhala upo wakumkola Iye m'kulankhula kwake.


Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu?


Tsiku lomwelo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; namfunsa Iye,


nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose;


Ndipo m'mawa mwake, ndilo tsiku lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhana kwa Pilato,


Pakuti ndinena ndi inu, ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.


Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?


Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake, namuyesa Iye.


Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa chinyengo chao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.


Ndipo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye, nanena,


Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?


Koma ena anamuyesa, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba.


Koma Iye anazindikira chinyengo chao, nati kwa iwo,


Ndipo anadza kwa Iye Asaduki ena, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye,


Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake.


Koma m'mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa ku Kachisi ndi Asaduki anadzako,


Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a chipatuko cha Asaduki, nadukidwa,


Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Agriki atsata nzeru:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa