Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 15:8 - Buku Lopatulika

8 Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 “ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutali ndi Ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “ ‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 15:8
11 Mawu Ofanana  

Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga.


Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patali ndi impso zao.


Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.


Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti,


Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine.


Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!


kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma Iye.


Ulibe gawo kapena cholandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa