Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 15:9 - Buku Lopatulika

9 Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Amandilambira Ine kwachabe ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 15:9
24 Mawu Ofanana  

Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m'manja mosalakwa.


Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.


Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.


ndipo mudzachita nayo mphamvu yanu chabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zake.


Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa chabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wake, ndi kuyenda ovala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?


Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse;


Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.


umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupirire chabe.


Chilichonse ndikuuzani, muchisamalire kuchichita; musamaonjezako, kapena kuchepsako.


kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'chikhulupiriro;


osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.


Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.


Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe?


Ndichita umboni kwa munthu aliyense wakumva mau a chinenero cha buku ili, Munthu akaonjeza pa awa, adzamuonjezera Mulungu miliri yolembedwa m'bukumu:


Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga chabe zake zonse za kaja kanali nazo m'chipululu, sikadasowe kanthu ka zake zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa