Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 15:14 - Buku Lopatulika

14 Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Alekeni, ndi atsogoleri akhungu ameneŵa. Tsono ngati wakhungu atsogolera wakhungu mnzake, onse aŵiri adzagwa m'dzenje.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Alekeni, ndi atsogoleri osaona. Ngati munthu wosaona atsogolera wosaona mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 15:14
19 Mawu Ofanana  

Koma Aejipito ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lake, wothandiza adzaphunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.


Ndani ali wakhungu, koma mtumiki wanga? Pena wagonthi, monga mthenga wanga, amene ndimtumiza? Ndani ali wakhungu monga bwenzi langa, ndi wakhungu monga mtumiki wa Yehova?


Alonda ake ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agalu achete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo.


Pakuti iwo amene atsogolera anthuwa, ndiwo awasokeretsa; ndipo iwo amene atsogoleredwa nao aonongeka.


aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?


Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita chonyansa? Iai, sanakhale konse ndi manyazi, sanathe kunyala; chifukwa chake adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika kwa iwo, adzagwetsedwa, ati Yehova.


Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.


Efuremu waphatikana ndi mafano, mlekeni.


Koma inu mwapatuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi, ati Yehova wa makamu.


Ndipo Iye ananenanso nao fanizo, Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzake wakhungu? Kodi sadzagwa onse awiri m'mbuna?


Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona.


makani opanda pake a anthu oipsika nzeru ndi ochotseka choonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa.


Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.


Aphunzitsi onamawo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira.


Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure:


Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa