Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 14:19 - Buku Lopatulika

19 Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Atatero, adalamula kuti anthu aja akhale pansi pa udzu. Tsono adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake, ophunzira aja nkukagaŵira anthuwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 14:19
24 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine.


Ndipo anawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulumagulu pamsipu.


Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo.


nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Efata, ndiko, Tatseguka.


Ndipo analandira chikho, ndipo pamene adayamika, anati, Landirani ichi, muchigawane mwa inu nokha;


Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.


Ndipo kunali m'mene Iye anaseama nao pachakudya, anatenga mkate, naudalitsa, naunyema, napatsa iwo.


Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye anati kwa ophunzira ake, Khalitsani iwo pansi magulumagulu, ngati makumi asanuasanu.


Ndipo Iye, m'mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang'ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo.


Pomwepo anachotsa mwala. Koma Yesu anakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.


koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pamalo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika;


Ndipo atanena izi, ndi kutenga mkate, anayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m'mene adaunyema anayamba kudya.


Iye wakusamalira tsiku, alisamalira kwa Ambuye: ndipo iye wakudya, adya mwa Ambuye, pakuti ayamika Mulungu; ndipo iye wosadya, mwa Ambuye sakudya, nayamikanso Mulungu.


Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi?


Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.


ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.


Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.


mutafika m'mzinda, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi ino mudzampeza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa