Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 14:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ake anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ake anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Nthaŵi yamadzulo ophunzira ake adadzamuuza kuti, “Kunotu nkuthengo, ndipo ano ndi madzulo. Auzeni anthuŵa azinyamuka, apite ku midzi kuti azikagula chakudya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 14:15
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesu pakumva, anachokera kumeneko m'ngalawa, kunka kumalo achipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kuchokera m'midzi.


Ndipo Iye anatuluka, naona khamu lalikulu la anthu, nachitira iwo chifundo, nachiritsa akudwala ao.


Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe chifukwa cha kumukira, apatseni ndinu adye.


Koma Iye sanamyankhe mau amodzi. Ndipo ophunzira ake anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu.


ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwao osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena a iwo achokera kutali.


Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumadera, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa