Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:57 - Buku Lopatulika

57 Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

57 Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

57 Choncho adakhumudwa naye. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao ndiponso kubanja kwao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

57 Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anawawuza kuti, “Mneneri sapatsidwa ulemu ku mudzi kwawo ndi ku nyumba kwawo.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:57
19 Mawu Ofanana  

Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala mu Yerusalemu.


Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.


Ndipo Iye, chifukwa cha kusakhulupirira kwao, sanachite kumeneko zamphamvu zambiri.


Ndipo Iye anatuluka kumeneko; nafika kudziko la kwao; ndipo ophunzira ake anamtsata.


Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.


Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.


Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m'nyumba yake.


Ndipo Iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika kudziko la kwao.


Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.


Pakuti Yesu mwini anachita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao.


Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?


Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung'ung'udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa