Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 13:5 - Buku Lopatulika

5 Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhale nalo dothi lakuya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya. Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga chifukwa nthakayo inali yosazama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 13:5
9 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;


Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu.


Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng'ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo;


Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwaa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.


Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera;


Ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nkulusira izo.


Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinafota.


Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera;


Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, chifukwa zinalibe nthaka yakuya;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa