Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 12:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Afarisi anatuluka, nakhala upo womchitira Iye mwa kumuononga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Afarisi anatuluka, nakhala upo womchitira Iye mwa kumuononga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo kuti apangane njira yophera Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Koma Afarisi anatuluka kunja ndi kukonza njira yoti amuphere.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 12:14
15 Mawu Ofanana  

nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi chinyengo, namuphe.


Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe;


Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:


Ndipo Afarisi anatuluka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye.


Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna maphedwe ake pakuti anaopa anthuwo.


Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzake kuti amchitire Yesu chiyani.


Ayuda anatolanso miyala kuti amponye Iye.


Anafunanso kumgwira Iye; ndipo anapulumuka m'dzanja lao.


Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe Iye.


Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye.


Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.


Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.


Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za Iye; ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire Iye.


Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja.


Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka mu Kachisi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa