Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 12:15 - Buku Lopatulika

15 Koma Yesu m'mene anadziwa, anachokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawachiritsa iwo onse,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma Yesu m'mene anadziwa, anachokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawachiritsa iwo onse,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Yesu atamva za upowo, adachokako kumeneko. Anthu ambiri adamtsatira, ndipo Iye adaŵachiritsa onse amene ankadwala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Podziwa zimenezi, Yesu anachoka kumalo amenewo. Ambiri anamutsata Iye ndipo anachiritsira odwala awo onse

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 12:15
15 Mawu Ofanana  

Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.


Ndipo makamu aakulu a anthu anamtsata; ndipo Iye anawachiritsa kumeneko.


Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena kumadera, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.


Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m'mitima yanu?


Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.


Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa.


Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake.


Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.


Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.


Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.


Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa