Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 11:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa mu Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa m'Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa iwe, achikhala zidaachitikira m'Sodomu, bwenzi mzindawo ukadalipo mpaka lero.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Ndipo iwe Kaperenawo, kodi udzakwezedwa kufika kumwamba? Ayi, udzatsitsidwa mpaka pansi kufika ku Hade. Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe, zikanachitika mu Sodomu, bwenzi iye alipo kufikira lero.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 11:23
30 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.


Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.


pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,


kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.


Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Ejipito, nuwagwetsere iye ndi ana aakazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.


Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.


Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.


Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo.


Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.


Ndipo pofika ku Kapernao amene aja akulandira ndalama za ku Kachisi anadza kwa Petro nati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo?


ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:


Ndipo m'mene Iye analowa mu Kapernao anadza kwa Iye kenturiyo, nampemba Iye,


Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku dziko la akufa.


Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.


Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake.


Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.


Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,


iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwe m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaone chivunde.


Monga Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.


ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.


Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala lamzinda waukulu, umene utchedwa, ponena zachizimu, Sodomu ndi Ejipito, pameneponso Ambuye wao anapachikidwa.


Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi dziko la akufa zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake.


Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa