Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 11:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Ndipo ngati mukufunadi kukhulupirira zimenezi, Yohaneyo ndiye Eliya uja ankati adzabwerayu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ndipo ngati inu mufuna kulandira izi, iyeyu ndi Eliya amene ankanena kuti adzabwera uja.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 11:14
12 Mawu Ofanana  

Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.


Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.


Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chinanenera kufikira pa Yohane.


Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.


Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.


Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simungachithe; ngakhale tsopano lino simungachithe; pakuti mulinso athupi;


Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa