Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 90:5 - Buku Lopatulika

5 Muwatenga ngati ndi madzi aakulu, akhala ngati tulo; mamawa akhala ngati msipu wophuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Muwatenga ngati ndi madzi aakulu, akhala ngati tulo; mamawa akhala ngati msipu wophuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Inu mumachotsa moyo wa anthu mwadzidzidzi. Ali ngati maloto, ali ngati udzu wongotsitsimuka m'maŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa, iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 90:5
16 Mawu Ofanana  

Adzauluka ngati loto, osapezekanso; nadzaingidwa ngati masomphenya a usiku.


Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao, chigumula chinakokolola kuzika kwao;


Kuyambira m'mawa kufikira madzulo athudzuka; aonongeka kosatha, osasamalirako munthu.


Apitirira ngati zombo zaliwiro; ngati mphungu igudukira chakudya chake.


Monga anthu atauka, apepula loto; momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa chithunzithunzi chao.


Pokhala panga pachotsedwa, pandisunthikira monga hema wa mbusa; Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba; Iye adzandidula ine poomberapo; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.


Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.


Mau a wina ati, Fuula. Ndipo ndinati, Kodi ndifuule chiyani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo;


udzu unyala, duwa lifota; chifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu.


Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa