Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 79:1 - Buku Lopatulika

1 Mulungu, akunja alowa m'cholowa chanu; anaipsa Kachisi wanu woyera; anachititsa Yerusalemu bwinja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mulungu, akunja alowa m'cholandira chanu; anaipsa Kachisi wanu woyera; anachititsa Yerusalemu bwinja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu Mulungu, anthu akunja aloŵerera m'dziko la anthu anu, aipitsa Nyumba yanu yoyera. Asandutsa Yerusalemu bwinja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowerera mʼcholowa chanu; ayipitsa Nyumba yanu yoyera, asandutsa Yerusalemu kukhala bwinja.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 79:1
25 Mawu Ofanana  

Natulutsa kuchotsa komweko chuma chonse cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolide adazipanga Solomoni mfumu ya Israele mu Kachisi wa Yehova, monga Yehova adanena.


Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake.


Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, naononga zipangizo zake zonse zokoma.


Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.


Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholowa chake.


Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka paphiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.


Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsere chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.


Anthu anu opatulika anakhala nacho kanthawi kokha; adani athu apondereza Kachisi wanu wopatulika.


Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.


Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu.


Tili ndi manyazi, chifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m'malo opatulika a nyumba ya Yehova.


ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.


Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.


Nati kwa iwo, Muipse nyumbayi ndi kudzaza mabwalo ndi ophedwa, mukani. Ndipo anatuluka, nakantha m'mzindamo.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa