Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 78:23 - Buku Lopatulika

23 Koma analamulira mitambo ili m'mwamba, natsegula m'makomo a kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Koma analamulira mitambo ili m'mwamba, natsegula m'makomo a kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Komabe Iye adalamula mitambo yamumlengalenga, natsekula zitseko zakumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba ndi kutsekula makomo a mayiko akumwamba;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:23
6 Mawu Ofanana  

Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.


ndipo kazembe uja adayankha munthu wa Mulunguyo, nati, Taonani tsono, Yehova angachite mazenera m'mwamba, chikachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ichi ndi maso ako, koma osadyako ai;


Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.


Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika.


ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isavumbwepo mvula.


Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa