Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 78:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo anawavumbitsira mana, adye, nawapatsa tirigu wa kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo anawavumbitsira mana, adye, nawapatsa tirigu wa kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Poŵagwetsera mana kuti adye, adaŵapatsa tirigu wakumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 anagwetsa mana kuti anthu adye, anawapatsa tirigu wakumwamba.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:24
10 Mawu Ofanana  

ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.


Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamane mana anu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao.


Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri, nawakhutitsa mkate wakumwamba.


Inu, Mulungu, munavumbitsa chimvula, munatsitsimutsa cholowa chanu pamene chidathodwa.


Ndipo atakamuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati chipale panthaka.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'chilamulo changa kapena iai.


nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi;


Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu; zovala zanu sizinathe pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinathe pa phazi lanu.


Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa