Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 77:2 - Buku Lopatulika

2 Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pa tsiku lamavuto ndimafunafuna Ambuye. Usiku wonse ndimakweza manja anga ndi kupemphera kosalekeza. Mtima wanga umakana kuusangalatsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye; usiku ndinatambasula manja mosalekeza ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 77:2
29 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.


Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.


Mukakhala njala m'dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala chinsikwi, kapena chinoni, dzombe, kapena kapuche; akawamangira misasa adani ao, m'dziko la mizinda yao; mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda iliyonse;


Ukakonzeratu mtima wako, ndi kumtambasulira Iye manja ako;


M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula, ndipo adzamva mau anga.


Pokumbukira Inu pa kama wanga, ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.


Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu; popeza mudzandivomereza.


Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala; koma ndani angatukule mtima wosweka?


Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.


Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.


Atero Yehova: Mau a amveka mu Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.


Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu.


Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.


Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Maria ananyamuka msanga, natuluka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa