Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 74:20 - Buku Lopatulika

20 Samalirani chipanganocho; pakuti malo a mdima a m'dziko adzala ndi zokhalamo chiwawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Samalirani chipanganocho; pakuti malo a mdima a m'dziko adzala ndi zokhalamo chiwawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Kumbukirani chipangano chanu, pakuti malo obisika am'dziko asanduka mochitira zankhanza zambirimbiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko asanduka mochitira zachiwawa zochuluka.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 74:20
19 Mawu Ofanana  

Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha, lolongosoka mwa zonse ndi losungika; pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse, ndi kufuma kwanga konse, kodi sadzachimeretsa?


Akumbukira chipangano chake kosatha, mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;


Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.


Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga.


Ndidzamsungira chifundo changa kunthawi yonse, ndipo chipangano changa chidzalimbika pa iye.


Munakaniza chipangano cha mtumiki wanu; munaipsa korona wake ndi kumponya pansi.


Musatinyoze ife, chifukwa cha dzina lanu; musanyazitse mpando wachifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.


Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.


Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo; musapenyerera kupulukira kwa anthu awa, kapena choipa chao, kapena tchimo lao;


Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa