Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 73:7 - Buku Lopatulika

7 Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao, malingaliro a mitima yao asefukira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao, malingaliro a mitima yao asefukira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Maso ao ndi otupa ndi kunenepa. Mitima yao ndi yodzaza ndi maganizo ofuna kuchita zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mʼmitima yawo yokhota mumachokera zolakwa; zoyipa zochokera mʼmaganizo awo sizidziwa malire.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 73:7
12 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu idati kwa Hamani, siliva akhale wako, ndi anthu omwe; uchite nao monga momwe chikukomera.


Popeza anakuta nkhope yake ndi kunenepa kwake, nachita mafunyenye a mafuta m'zuuno zake;


Mtima wao unona ngati mafuta; koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu.


Mafuta ao awatsekereza; m'kamwa mwao alankhula modzikuza.


kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.


Tapenyani, oipa ndi awa; ndipo pokhazikika chikhazikikire aonjezerapo pa chuma chao.


Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha.


Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.


Taona, mphulupulu ya mng'ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa.


Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wake anali ku Karimele; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi chikwi chimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zake ku Karimele.


Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuze kanthu konse, kufikira kutacha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa