Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 73:16 - Buku Lopatulika

16 Pamene ndinayesa kudziwitsa ichi, ndinavutika nacho;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pamene ndinayesa kudziwitsa ichi, ndinavutika nacho;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Koma pamene ndidalingalira zimenezi kuti ndizimvetse bwino, zidandiwonekera ngati nkhani yovuta,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Pamene ndinayesa kuti ndimvetse zonsezi, zinandisautsa kwambiri

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 73:16
10 Mawu Ofanana  

Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Njira yanu inali m'nyanja, koyenda Inu nkumadzi aakulu, ndipo mapazi anu sanadziwike.


Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wake wachifumu.


Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.


pamenepo ndinaona ntchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole ntchito zichitidwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola.


Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa