Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 69:36 - Buku Lopatulika

36 Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira; ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m'mwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira; ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m'mwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Ana a atumiki ake nawonso adzalilandira kuti likhale lao, ndipo okonda Mulungu adzakhala m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo, ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 69:36
13 Mawu Ofanana  

Ana a atumiki anu adzakhalitsa, ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.


Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.


Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.


Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.


Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa.


Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.


Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.


Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.


Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa