Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 49:16 - Buku Lopatulika

16 Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Usavutike munthu wina akamalemera, pamene chuma cha m'nyumba mwake chikukulirakulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Usavutike mu mtima pamene munthu akulemera, pamene ulemerero wa nyumba yake ukuchulukirachulukira;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 49:16
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse.


Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.


Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama.


Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.


Ndidzaoperanji masiku oipa, pondizinga amphulupulu onditsata kuchidendene?


Posekera olungama pali ulemerero wambiri; koma pouka oipa anthu amabisala.


Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.


Ndipo amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwake; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.


ndipo adzatenga ulemerero ndi ulemu wa amitundu nadzalowa nao momwemo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa