Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 44:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Iwo sadalande dziko ndi lupanga lao, sadapambane pa nkhondo ndi mphamvu zao. Koma adagonjetsa ndi mphamvu zanu, chifukwa cha kuŵala kwa nkhope yanu, pakuti mudakondwera nawodi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Sanalande dziko ndi lupanga lawo, si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso, koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu, pakuti munawakonda.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 44:3
27 Mawu Ofanana  

Ndiponso mtundu uti wa padziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao?


Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pamaso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?


Anaonetsera anthu ake mphamvu ya ntchito zake, pakuwapatsa cholowa cha amitundu.


Onetsani chifundo chanu chodabwitsa, Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.


Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake; adzamvomereza mu Mwamba mwake moyera ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja.


Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.


Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu? Mulitulutse kuchifuwa chanu ndipo muwatheretu.


Munaombola anthu anu ndi mkono wanu, ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe.


Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao.


Unapserera ndi moto, unadulidwa; aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.


Mudasoseratu pookapo, idagwiritsa mizu yake, ndipo unadzaza dziko.


Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola.


amene anayendetsa mkono wake waulemerero padzanja lamanja la Mose? Amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha?


Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.


Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.


Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;


Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino.


Ndipo ndinatuma mavu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai.


Nati Yoswa, Ndi ichi mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapirikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa