Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 44:12 - Buku Lopatulika

12 Mugulitsa anthu anu kwachabe, ndipo mtengo wake simupindula nao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Mugulitsa anthu anu kwachabe, ndipo mtengo wake simupindula nao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Inu mwagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika, ndipo simudapindulepo kanthu ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika, osapindulapo kanthu pa malondawo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 44:12
10 Mawu Ofanana  

Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.


Chuma chako ndi zosungidwa zako ndidzazipereka zifunkhidwe kopanda mtengo wake, ichicho chidzakugwera chifukwa cha zochimwa zako zonse, m'malire ako onse.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.


ndi sinamoni ndi amomo, ndi zofukiza, ndi mure, ndi lubani, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magaleta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele ndipo anawagulitsa m'dzanja la Kusani-Risataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israele anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa