Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 44:11 - Buku Lopatulika

11 Mwatipereka ngati nkhosa zoyenera kuzidya; ndipo mwatibalalitsa mwa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Mwatipereka ngati nkhosa zoyenera kuzidya; ndipo mwatibalalitsa mwa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Inu mwatisandutsa nkhosa zokaphedwa, mwatibalalitsa pakati pa mitundu ina ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 44:11
13 Mawu Ofanana  

Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa mu Hala, ndi mu Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'mizinda ya Amedi.


Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko.


Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova.


Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; mwakwiya; tibwezereni.


Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.


Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,


Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


Monganso kwalembedwa, Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwe, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala.


Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa