Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 40:9 - Buku Lopatulika

9 Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu; onani, sindidzaletsa milomo yanga, mudziwa ndinu Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu; onani, sindidzaletsa milomo yanga, mudziwa ndinu Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndalalika uthenga wabwino wa chipulumutso chanu pa msonkhano waukulu. Sindidatseke pakamwa, monga mukudziŵa, Inu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu; sinditseka milomo yanga monga mukudziwa Inu Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 40:9
14 Mawu Ofanana  

Ndinafotokozera ndi milomo yanga maweruzo onse a pakamwa panu.


Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.


Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.


Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.


Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu; m'chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani.


Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake; pakuyenda pake sadzaterereka.


Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;


Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga.


Ndi kuti, Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuimbirani.


Yehova Chauta Mulungu, Yehova Chauta Mulungu, Iye adziwa, ndi Israele adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa