Masalimo 40:10 - Buku Lopatulika10 Chilungamo chanu sindinachibise m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisire msonkhano waukulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Chilungamo chanu sindinachibisa m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisira msonkhano waukulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga; ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu. Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu pa msonkhano waukulu. Onani mutuwo |