Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 38:19 - Buku Lopatulika

19 Koma adani anga ali ndi moyo, nakhala ndi mphamvu, ndipo akundida kopanda chifukwa achuluka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Koma adani anga ali ndi moyo, nakhala ndi mphamvu, ndipo akundida kopanda chifukwa achuluka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ngamphamvu adani amene amafuna moyo wanga, ngambiri amene amandida popanda chifukwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ambiri ndi adani anga amphamvu; amene amandida popanda chifukwa alipo ochuluka kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 38:19
11 Mawu Ofanana  

Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu, ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.


Penyani adani anga, popeza achuluka; ndipo andida ndi udani wachiwawa.


Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine! Akundiukira ine ndi ambiri.


Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.


Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.


Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.


Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa