Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 33:12 - Buku Lopatulika

12 Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao; mtundu womwe anausankha ukhale cholowa cha Iye yekha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao; mtundu womwe anausankha ukhale cholandira cha Iye yekha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ngwodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta, anthu amene Chauta waŵasankha akeake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova, anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 33:12
17 Mawu Ofanana  

Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?


Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo, Israele, akhale chuma chake chenicheni.


Odala anthu akuona zotere; odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova.


Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholowa chanu; muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.


Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.


Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.


monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.


Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake.


Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.


amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa