Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:29 - Buku Lopatulika

29 Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Onenepa onse a pa dziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Anthu onse odzitama adzamuŵeramira. Anthu onse oloŵa m'manda nawonso adzamugwadira, ndiye kuti onse osatha kudzisungira moyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira; onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake; iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:29
20 Mawu Ofanana  

Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi, nakweza waumphawi kumchotsa kudzala.


Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.


Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao, malingaliro a mitima yao asefukira.


pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira, ndipo anapha mwa onenepa ao, nagwetsa osankhika a Israele.


Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.


Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.


Ndipo iwe udzagwetsedwa pansi, nudzanena uli pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala pansi kotuluka m'fumbi; ndi mau ako adzakhala ngati a wina amene ali ndi mzimu wobwebweta, kuchokera pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala konong'ona kochokera m'fumbi.


Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.


Iwe udzayamwanso mkaka wa amitundu, nudzayamwa bere la mafumu, nudzadziwa kuti Ine Yehova ndine Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu ya Yakobo.


Israele, chikuononga ndi ichi, chakuti utsutsana ndi Ine, chithandizo chako.


Ndipo apulumutsi adzakwera paphiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wake wa Yehova.


Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.


kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko,


Ndipo amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwake; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa