Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 22:26 - Buku Lopatulika

26 Ozunzika adzadya nadzakhuta, adzayamika Yehova iwo amene amfuna, ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ozunzika adzadya nadzakhuta, adzayamika Yehova iwo amene amfuna, ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Ozunzika adzadya ndi kukhuta, ofunafuna Chauta adzamtamanda. Ine ndidzati, “Mitima yanu ikhale ndi moyo nthaŵi zonse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Osauka adzadya ndipo adzakhuta; iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda. Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 22:26
15 Mawu Ofanana  

Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.


Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka, nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.


Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse.


Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse.


Chilungamo chanu sindinachibise m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisire msonkhano waukulu.


Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova.


Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko; numchitire Wam'mwambamwamba chowinda chako.


Ofatsa anachiona, nakondwera, ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo.


Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi;


Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.


koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa