Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 18:17 - Buku Lopatulika

17 Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu, ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu, ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu, kwa onse amene ankadana nane, pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga, amene anali amphamvu kuposa ine.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 18:17
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo.


Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu.


Iye ananding'amba m'kundida kwake, nakwiya nane, anandikukutira mano; mdani wanga ananditong'olera maso ake.


Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza; m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.


Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.


Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri; ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andipambana.


Tulutsani manja anu kuchokera m'mwamba; ndikwatuleni ndi kundilanditsa kumadzi aakulu, kudzanja la alendo;


Penyani adani anga, popeza achuluka; ndipo andida ndi udani wachiwawa.


Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?


Koma adani anga ali ndi moyo, nakhala ndi mphamvu, ndipo akundida kopanda chifukwa achuluka.


Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa.


Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa