Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 119:141 - Buku Lopatulika

141 Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa; koma sindiiwala malemba anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

141 Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa; koma sindiiwala malemba anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

141 Ine ndine wamng'ono ndi wonyozeka, komabe sindiiŵala malamulo anu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

141 Ngakhale ndili wamngʼono ndi wonyozeka, sindiyiwala malangizo anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:141
14 Mawu Ofanana  

Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu.


Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu.


Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu.


Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu.


Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga.


Zapang'ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.


Zapang'ono, pokhala chilungamo, ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo.


Wosauka woyenda mwangwiro aposa wokhetsa milomo ndi wopusa.


Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga;


Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Ndipo Iye anakweza maso ake kwa ophunzira ake, nanena, Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.


Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe zili nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu.


Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa