Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 109:7 - Buku Lopatulika

7 Ponenedwa mlandu wake atuluke wotsutsika; ndi pemphero lake likhale ngati kuchimwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ponenedwa mlandu wake atuluke wotsutsika; ndi pemphero lake likhale ngati kuchimwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Pomuweruza apezeke kuti ali ndi mlandu, mapemphero ake akhale ngati kupalamula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Pamene aweruzidwa, apezeke kuti ndi wolakwa, ndipo mapemphero ake amutsutse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 109:7
9 Mawu Ofanana  

Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.


Nsembe ya oipa inyansa; makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu.


Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.


Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa