Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 109:12 - Buku Lopatulika

12 Pasakhale munthu wakumchitira chifundo; kapena kuchitira chokoma ana ake amasiye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pasakhale munthu wakumchitira chifundo; kapena kuchitira chokoma ana ake amasiye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima, kapena wina woŵachitira chifundo ana ake amasiye aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima kapena kumvera chisoni ana ake amasiye.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 109:12
9 Mawu Ofanana  

Ana ake akhala otekeseka, napsinjika kuchipata, wopanda wina wakuwapulumutsa.


Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzachitira chisoni chipatso cha mimba; diso lao silidzaleka ana.


Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.


Chifukwa chake Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wochimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.


Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.


Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa