Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 104:5 - Buku Lopatulika

5 anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka kunthawi yonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka kunthawi yonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mudakhazika dziko lapansi pa maziko ake, kuti lisagwedezeke konse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake; silingasunthike.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 104:5
14 Mawu Ofanana  

Ayala kumpoto popanda kanthu, nalenjeka dziko pachabe.


Chikhulupiriko chanu chifikira mibadwomibadwo; munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.


Amene anayala dziko lapansi pamwamba pamadzi; pakuti chifundo chake nchosatha.


Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi.


Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika.


Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.


Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.


Poikira nyanja malire ake, kuti madzi asapitirire pa lamulo lake; polemba maziko a dziko.


Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.


Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Ndipo kumwamba kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kuchoka m'malo mwao.


Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa