Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 9:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye anawalamula kuti asauze munthu zinthu zimene adaziona, koma pamene Mwana wa Munthu akadzauka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye anawalamula kuti asauze munthu zinthu zimene adaziona, koma pamene Mwana wa Munthu akadzauka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Pamene ankatsika phirilo, Yesu adaŵaletsa kuti zimene adaaonazo asauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pamene ankatsika kuchokera ku phiri, Yesu anawalamulira kuti asawuze aliyense zimene anaona mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.

Onani mutuwo Koperani




Marko 9:9
15 Mawu Ofanana  

Sadzalimbana, sadzafuula; ngakhale mmodzi sadzamva mau ake m'makwalala;


pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.


Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.


nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu.


Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.


Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.


Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu aliyense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana.


Ndipo anasunga mauwo, nafunsana mwa iwo okha, kuti, Kuuka kwa akufa nchiyani?


Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenye munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.


ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;


Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu aliyense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa