Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 9:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mzimu umenewu wakhala ukumugwetsa kaŵirikaŵiri, mwina amagwa pa moto, mwina m'madzi, kufuna kumupha. Koma ngati Inu mungathe kuchitapo kanthu, chonde tatichitirani chifundo, mutithandize.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 9:22
12 Mawu Ofanana  

Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima?


Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala khunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi.


Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.


Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza.


Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.


Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo.


Ndipo Iye anafunsa atate wake, kuti, Chimenechi chinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Chidamyamba akali mwana.


Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.


Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa