Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 9:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo Iye anafunsa atate wake, kuti, Chimenechi chinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Chidamyamba akali mwana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo Iye anafunsa atate wake, kuti, Chimenechi chinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Chidamyamba akali mwana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Yesu adafunsa bambo wake uja kuti, “Kodi zimenezi zidamuyamba liti?” Bambo wakeyo adati, “Zidamuyamba ali mwana ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Yesu anafunsa abambo a mnyamatayo kuti, “Kodi wakhala chotere nthawi yayitali bwanji?” Iye anayankha kuti, “Kuyambira ali wamngʼono,

Onani mutuwo Koperani




Marko 9:21
15 Mawu Ofanana  

Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto.


Koma munthu abadwira mavuto, monga mbaliwali zikwera ziuluzika.


Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.


Ndipo munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri,


Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsa; ndipo anagwa pansi navimvinika ndi kuchita thovu.


Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.


Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata?


Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense,


Ndipo popita, anaona munthu ali wosaona chibadwire.


Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayende nthawi zonse.


Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa mu Kachisi;


Pakuti anali wa zaka zake zoposa makumi anai munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidachitidwa kwa iye.


Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa