Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 5:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Yesu adailoladi. Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo. Zonse zidaalipo ngati zikwi ziŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira.

Onani mutuwo Koperani




Marko 5:13
12 Mawu Ofanana  

Nati, Ndidzatuluka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; tuluka, ukatero kumene.


Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Taona, akhale m'dzanja lako; moyo wake wokha uuleke.


Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.


Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi.


Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo.


Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mzinda, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho.


Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.


amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yake;


Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake mu Chihebri Abadoni, ndi mu Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa