Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 4:41 - Buku Lopatulika

41 Ndipo iwo anachita mantha aakulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Ndipo iwo anachita mantha akulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Koma iwo adaagwidwa ndi mantha kwambiri, nkumafunsana kuti, “Kodi Iyeyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”

Onani mutuwo Koperani




Marko 4:41
17 Mawu Ofanana  

ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo; apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?


Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.


Chipangano changa chinali naye cha moyo ndi cha mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa chifukwa cha dzina langa.


Ndipo pamene iwo analowa m'ngalawamo, mphepo inaleka.


Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?


Ndipo ananena nao, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi?


Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, kudziko la Agerasa.


Koma mkaziyo anachita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa chimene anamchitira iye, nadza, namgwadira, namuuza choona chonse.


Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.


Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Chikhulupiriro chanu chili kuti? Ndipo m'kuchita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye?


Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha.


Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.


Koma mumuope Yehova, ndi kumtumikira koona, ndi mtima wanu wonse; lingalirani zinthu zazikuluzo Iye anakuchitirani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa